CHIDZIWITSO: Bungwe la UNDP lithandiza pa ndondomeko yowona masamalidwe a zotsatira za zisankho

May 9, 2014

Ngati mbali imodzi ya pulogalamu yake yothandizira bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC), bungwe la United Nations Development Programme (UNDP) lapereka mwai ku kampani ina ya mudziko muno yotchedwa Globe Computer Systems Limited kuti ipange makina omwe adzigwiritsidwa pa ntchito yosamalira zotsatira za zisankho. Thandizo la ntchitoyi likupelekedwa kudzera mu thumba la ndalama lomwe mabungwe osiyana siyana akunja amene amathandiza dziko lino aika pamodzi lomwe pa chingelezi likutchedwa kuti Basket Fund.

Makina amenewa akupangidwa kumene osati kapena kuchokera pa makina ena ali onse omwe adalipo kale mbuyomu. Izi zili choncho polimbikitsa malamulo omwe bungwe la MEC latenga pofuna kuonetsetsa kuti chisankho chikhale cha bata ndi chilungamo. Kusiyana ndi mmene zisankho zimachitikira mbuyomu, pamene makina a telephone aja pachizungu amatchedwa kuti fax machine amagwiritsidwa ncthito potumiza zotsatira za zisankho, makina atsopanowa adzagwritsa ntchito njira yamakono ya internet potenga zotsatira za zisankho kuchokera kumadera onse adziko lino. Makinawa adzagwiritsidwa ncthito ndi a bungwe la MEC powonetsetsa kuti zotsatira za zisankho zikutumizidwa mwansanga komanso motetezedwa kukafika ku malo komwe zotsatirazi zizawelengedwe, komwe pa chingelezi kumatchedwa ku National Tally Centre.

Komanso, kagwiritsidwe ntchito ka makinawa kadzathandizanso kuzindikira ngati pali chinyengo china chili chonse chomwe chachitika pa zasinkhozi. Makina atsopanowa, alinso ndi ukadaulo otha kuzindikira ngati panapangika kena kali konse pofuna kubela zisankhozi pogwiritsa ntchito njira zakale zakatetezedwe ka zotsatira za zisankhozi komanso kutha kutsata ndondomeko yonse yowonkhetsera zotsatirazi ndikuona ngati pali zolakwika zili zonse pa kaonkhwetsedweko.

Kampani ya Globe inasankhadwa podzera ndondomeko yomwe makampani ambiri anaonetsa nawo chidwi chopeza mwayi opanga ntchitoyi. Kampaniyi inasankhidwa kamba kokuti inali ndi zonse zowayenereza kugwira ncthitoyi. Makinawa akupangidwa moyang’aniridwa ndi a bungwe la MEC ndiponso la UNDP, ndipo akhala akuyesedwa mwatsatanetsatane kuti awone ngati akugwira ncthito moyenera. Malingana ndi ndondomeko yomwe a MEC akugwiritsa ntchito powona kuti palibe chinyengo cha mtundu wina uli onse chomwe chikuchitika, makinawa adzawayesanso pamaso pa zipani zonse ndinso mabungwe ena onse omwe akutenga nawo mbari pa nkhani ya zisankhozi tsiku la chisankho lisadafike.

UNDP Around the world

You are at UNDP Malawi 
Go to UNDP Global